Zilonda ZapakhunguпјгGg i.s
Zilonda Zapakhungu Magulu ndiponso kumene kwachokera zinthu Chilonda chachikulu chapakhungu padzanja la munthu wamkulu ndithu ku Central America ICD/CIM-10 B55 B55 ICD/CIM-9 085 085 DiseasesDB 3266 MedlinePlus 001386 Zilonda zapakhungu zomwe pa Chingelezi zimatchedwa Leishmaniasis kapenanso leishmaniosis , ndi matenda amene amayambitsidwa ndi tizilombo ta m'gulu la mapulotozowa otchedwa Leishmania ndipo tizilomboti zimafalitsidwa ndi ntchentche zinazake zoluma. [1] Matendawa angagawidwe m'magulu atatu: zilonda zazikulu, zilonda zamafinya, ndiponso zilonda zapakhungu la ziwalo za mkati mwathupi. [1] Matenda a m'gulu loyambalo amadziwika chifukwa cha kukula kwa zilonda zake, pomwe a m'gulu lachiwirilo amadziwika ndi zilonda zamafinya pakhungu, m'kamwa ndiponso m'phuno, pomwe gulu lomalizalo limadziwika ndi zilonda zapakhungu, kuphwanya thupi, kuchepa kwa masero ofiira m'thupi, ndiponso kutupa kwa kapamba ndi chiwindi. [1] [2] Matendawa amafali...